Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Politics

Boma lipitiriza kufikitsa zitukuko mmadera onse — Chimwendo Banda

Mkulu wa achinyamata m’chipani cha Malawi Congress (MCP) yemwenso ndi nduna ya maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, walangiza anthu amdera lakuzambwe m’boma la Mangochi kuti apitirize kukhala pambuyo pa chipani cha MCP ndi mtsogoleri wake Dr Lazarus Chakwera kuti chitukuko chipitilire m’dziko muno.

Poyankhula pa sukulu ya pulaimale ya Chamtulo mdela la Senior Chief Nankumba, a Chimwendo Banda anatsimikizira khwimbi la anthu lomwe linasonkhana pabwaloli kuti boma lipitiliza kupeleka ndalama zamtukula pakhomo kwa anthu pofuna kuthana ndi mavuto osiyanasiyana omwe akukumana nawo.

Iwo anatsindikanso kuti posachedwapa boma liyamba kumanga msewu wa Chilipa kupita ku Balaka.

A Chimwendo Banda omwe anayankhulanso mu chiyao chomveka bwino kuti anthu panopa adazindikira ndipo palibe amene angabwere kudzawanamizanso.

Poyankhula poyambilira wachiwiri wina kwa mlembi wa chipani cha MCP, a Gerlad Kazembe, anati ndizosangalatsa kuti anthu a m’boma la Mangochi amvana chimodzi pokhala pambuyo pa Prezidenti Chakwera.

Akulu akulu wosiyanasiyana a chipani cha MCP, aphungu anyumba ya malamulo komanso mafumu ndi ena ambiri anali nawo pa msonkhanowu.

 

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

CROSS-BORDER TRADERS DONATE TO THYOLO HOSPITAL

MBC Online

ECD SERVICES REACH 2 MILLION CHILDREN

McDonald Chiwayula

POLICE APPREHEND HEALTH WORKER OVER ALLEGED RAPE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.