Boma latsimikizila alimi mdziko muno kuti asade nkhawa za misika komwe akagulitse mbewu zao.
Nduna ya zaulimi a Sam Kawale anena izi atayendela alimi omwe apindula ndi ngongole za ulimi za NEEF.
A Kawale ati kampani zambili kuphatikizapo ya Pyxus ndi Paramount Holdings zatsimikizila boma kuti agula mbewu zochuluka kuchokera kwa alimi chaka chino.
Iwo ati pali mwai waukulu kuti nalo bungwe la ADMARC liyamba kugula mbewu mu nthawi yake kaamba koti nduna yoona zachuma yawatsimikila zakuthekera kopereka ndalama zokwanira ku bungweli.
Alimi ambiri omwe awayendera kale m’maboma a Lilongwe, Mchinji ndi Ntchisi akuyamika boma chifukwa chopereka ngongole za NEEF kwa alimi ponena kuti zikuwapatsa mwai wogula zipangizo zambiri zaulimi poyerekeza ndi ndondomeko ya AIP.
M’modzi mwa alimiwa, a Bonface Puye, m’boma la Mchinji ati ngongole za NEEF zitafikila alimi ambili mdziko muno nkhani ya njala itha kukhala mbili ya makedzana.
Ndipo poyankhula kwa Mkanda a Kawale atsimikira alimi omwe sanagule fetereza kuti aonetsetsa kuti akupezeka mosavuta.
Phungu wadera la kumpoto m’boma la Mchinji, a Rachel Mazombwe Zulu, ayamika boma la Dr Lazarus Chakwera chifukwa choika chidwi pa ulimi zomwe ati zithandiza kuthetsa vuto la njala.
Wolemba Mayeso Chikhadzula.