Boma la United States, kudzera ku bungwe la USAID, lapereka K12 billion ku boma la Malawi kuti zithandizire anthu amene akhudzidwa ndi njala.
Polengeza za thandizoli, a Pamela Fessenden, omwe ndi mkulu wa USAID Malawi, ati izi zikutsatira kulengeza kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti maboma 23 mwa maboma 28 ali pa ngozi ya njala m’dziko muno.
Iwo ati apitiriza kuthandiza boma la Malawi mu njira zosiyanasiyana.
Olemba: Blessings Cheleuka