Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Blue Eagles yayamba moyo wa ligi ya Chipiku ndichipambano

Timu ya Blue Eagles, yomwe idatuluka mu ligi yaikulu chaka chatha, yayamba ulendo wake wa ligi ya m’chigawo chapakati ya Chipiku ndi chimwemwe pomwe yathambitsa Dzaleka Future ndi zigoli zinayi kwa duu pamasewero otsekulira ligiyi amene anachitikira pabwalo la zamasewero la Dowa.

Andrew Juvinala ndiyemwe anayamba kuliza mfuti mgawo loyamba Tonic Viyuyi asalize mizinga iwiri yekha motsatizana kuti apolisi aku Area 30 wa akhwimitse chitetezo pabwaloli.

Schumaker Kuwali ndiyemwe anamalizitsa perete wa apolisiwa pomwe anamwetsa chigoli chapamwamba atadyetsa njomba anyamata otchinga kumbuyo aku Dzaleka wa ndikubvumbulutsa mzinga wamphamvu kuti nkhwazizi ziyambe ndikuuluka mwachiwemwe.

Mphuzitsi wa Blue Eagle, Eliya Kananji, wati timu ikaphweka zimafunika kuchitiratu ndipo wati ayesetsa kuti apitirize momwe ayambira kuti mwayi wawo obwelera mu ligi yaikulu ukhale osakaikitsa.

Mlembi wamkulu wa bungwe loyendetsa masewero ampira wamiyendo mchigawo chapakati, Antonio Manda, wati ligiyi yayamba bwino ndipo ayesetsa kuti iyende mwaukadaulo.

Pamwambowu panalinso mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, yemwe wapempha mabungwe oyendetsa mpira m’zigawo zonse kuti aonetsetse kuti ma ligi awo athe munthawi yabwino komanso yofanana.

Ligi ya Chipiku ikuthandizidwa ndi ndalama zokwana K19.8 million ndipo masewero akhale akupitilira sabata ya mawa.

 

Olemba: Foster Maulidi

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Inflation likely to ease — Finance Minister

Earlene Chimoyo

CABINET RESHUFFLE

McDonald Chiwayula

52 Ethiopian nationals arrested for illegal entry

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.