Anthu awiri afa ku Thyolo potsatira zipolowe zomwe zinadza kutsatira mikangano ya ufumu wa Mankhamba pakati pa mayi Elizabeth Paulo komanso Laison Folopezi.
Zipolowezi zinayambika pamene mwambo olowetsa ufumu umayamba lachiwiri m’bomali pamene anthu okwiya akwa Mankhamba anagenda ndi miyala komanso kuwagwira a Gulupu James Ndipo anafera pomwepo.
Izi zitachitika, gulu lambali inayo linapita mudzi winawo ndikugwira a John Keliyasi ndi kuwagenda ndipo nawonso afa.
Pakadali pano, wofalitsa nkhani zapolisi ku chigawo chakummwera, a Edward Kabango, ati apolisi akufufuza nkhaniyi.
DC wa m’bomali, a Hudson Kuphanga, wati ndizodadandaulitsa kuti mikanganoyi ikuchitika m’bomalo.
Mkangano wa ufumu wa Mankhamba unayamba mu 2013 ndipo nkhaniyi yakhala ikupita ku khothi. Mu 2016, khothi linapereka chiletso kuti awunikire za yemwe akuyenera kukhala mfumu.
Pa 1 September 2017, chiletsochi chinachotsedwa kuti Mfumu Thomas itha kugwira ntchito ngati Mfumu ya ndodo ndipo ndiwoyenelera kulowetsa ufumu.
Ngakhale zinali choncho, mayi Paulo sanakhutire ndi chigamulochi ndipo anauza ogwira ntchito ku ofesi ya DC kuti achita chotheka kulepheretsa mwambo odzodza ufumu ndipo sanamvere langizo lakuti apite kwa loya wawo kuti atengere nkhaniyi ku khothi lalikulu.