Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Awamanga ataba mabisiketi ku kampani ya Universal

Apolisi ku Area 36 ku Lilongwe amanga anthu atatu powaganizira kuti anathyola ndikuba katundu wa mnyumba wa ndalama pafupifupi K7.5 million, kenako usiku womwewo anakaba mabisiketi ku kampani ya Universal Industries.

Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati anthuwo ndi Yamikani Sosten wazaka 32 yemwe amadziwikanso kuti “Short”, Martin Lukiya wazaka 38 ndi  Dominic Gilbert wazaka 35.

A Chigalu ati apolisi anapita kunyumba kwa mbavazo akuluakulu a kampani ya Universal Industries atakapereka lipoti ku ofesi yawo.

Atafika kunyumbako, apolisiwo anapezanso katundu wina wamnyumba yemwe mbavazo zinaulula kuti zinakaba ku Area 36 ndipo mwini nyumbayo anali asanadziwe kuti kunyumba kwake kwabedwa, ngakhale panali patadutsa tsiku limodzi.

A Chigalu anatsimikiza kuti mwini nyumbayo sanadziwedi kanthu mpaka pomwe apolisiwo anapita kukamudziwitsa kuti waberedwa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Zambia appreciates Malawi’s irrigation scheme initiatives

MBC Online

NGOs urged to embrace social enterprise

Simeon Boyce

Man gets 18 years for raping stepdaughter

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.