Apolisi ku Soche mumzinda wa Blantyre amanga amuna ena awiri, kuphatikiza pa atatu omwe anawagwira kale mwezi wa March, pa mlandu wakuba ndikuvulaza munthu ku Soche East mumzinda womwewo.
Ofalitsankhani wapolisi ku Soche, Aaron Chilala, wati awiriwo, omwe awagwira ku Nsanje komwe amabisala, ndi John Washen wazaka 57 ndi James Basopa wazaka 37, ndipo awapezanso ndi zipolopolo 12.
A Chilala ati awiriwo, pamodzi ndi ena atatu omwe akuwasunga ku ndende ya Chichiri, anapita kunyumba ya Alex Makanjira ku Soche East, omwe anawaombera ndi mfuti yamtundu wa AK-47 kenako anaba katundu wa mnyumba ndi ndalama zokwana K100, 000.
Apolisi anakwanitsa kupeza katundu wina wobedwayo komanso anapeza mfuti yomwe anthuwo amagwiritsa ntchito.