Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Athokoza asilamu popemphelera dziko lino mu nyengo ya Ramadhan

Phungu wa dera la Lilongwe City South East a Ulemu Msungama wathokoza asilamu popemphelera magawo osiyanasiyana a dziko lino mu nyengo yosala kudya ndi kupemphera ya Rhamadhan.

A Msungama anena izi pa sukulu ya Mlodza ku Lilongwe pomwe amapereka mphatso ya zakudya zosiyanasiyana kwa amayi a masiye ndi ena osowa ochokera mu mizikiti ya mdera lawo, ngati mbali imodzi yowathandizira kuti athe kusangalala nawo pamene akumaliza mwezi wa kusala kudya wa Ramadhan.

“Kusala kudya ndi kupemphera kumeneku kuli ndi tanthauzo lalikulu mdziko muno. Anthu amenewa amapemphelela dziko lathu pa nkhani za chuma mabizinesi sukulu komanso mabanja. Mukaona izi ndi zimene a Prezidenti athu amatilimbikitsa,” anatelo a Msungama.

Asilamu akhala akusala kudya ndipo akuyembekezeka kumaliza kupemphera ndi kusala kudyaku ndi kukondwelera Eid Ul Fitr mwezi ukatuluka tsiku lililonse sabata ino.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Bus ya Bullets inakalibe mmanja mwa khothi

MBC Online

TNM ipereka mabandulo aulere kwa makasitomala ake popilira kuvuta kwa internet

MBC Online

Adakali mu ululu

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.