Asilikali ankhondo adziko lino a MDF, pamodzi ndi nthambi zina za chitetezo, akufunafunabe ku Chikangawa m’boma la Mzimba ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima.
Asilikaliwa komanso a polisi pano akupita ku Thungwa m’dera lomweli la chikangawa kukayang’ana ndegeyi.
Ndegeyi inanyamula Dr Chilima ndi akuluakulu ena asanu ndi anayi ndipo inasowa dzulo lolemba mu nkhalango ya Chikangawa, malinga ndi malipoti ochokera ku MDF.
Dr Chilima anali pa ulendo opita kumaliro a malemu Raphael Kasambara, amene aikidwa m’manda dzulo ku mudzi kwawo ku Nkhatabay.
Ndengeyo inakanika kutera pa bwalo la ndege la Mzuzu kaamba ka mitambo ndipo yasowa panthawi imene imabwelera ku Lilongwe.
Pakadali pano, mtsogoleri wa dziko lino wapempha thandizo kuchokera ku maiko ena akunja monga America, Norway, Britain komanso Israel pa ntchito yofufuza ndegeyi ndipo maikowa avomera kale.
Ena mwa akuluakulu omwe anakwera mu ndegeyi ndi a Shanil Dzimbiri, Abdul Lapukeni, Lukas Kapheni, Chisomo Chimaneni, Gloria Mtukule, Colonel Sambalopa, Major Aidini komanso Major Selemani.
Olemba: Jackson Sichali