Apolisi ku Soche mu mzinda wa Blantyre amanga alonda awiri a kampani ya zomangamanga ya AFECC komanso anthu atatu ochita malonda pa sitolo ya hardware powaganizira kuti anaba katundu womangira bwalo la masewero la timu ya Mighty Mukuru Wanderers wa ndalama zokwana K10 million.
Malinga ndi a Aaron Chilala amene ndi ofalitsankhani pa polisi ya Soche, anthuwa analongedza katunduyo mu galimoto koma apolisi anawagwira pamene amafuna adzituluka pamalopo.
Anthuwa: Nedson Pondani, 66 ndi Patrick Lime, 40 omwe ndi alonda komanso Weston Manyong’onya, 42, Henry Chanza, 41 ndi Rodgers Malembo, 42 omwe amachita malonda a hardware, ali mu chitokosi ndipo akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu okuba.
Olemba : Charles Pensulo