Apolisi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre amanga anthu anayi atapezeka ndi ndalama zachinyengo zokwana K915,000.
M’neneri wa polisi ya Chileka, a Jonathan Phillipo, wati apolisiwo akwanitsanso kulanda makina amene anthuwo amagwiritsa ntchito popanga ndalama zachinyengozo.