Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local Local News Nkhani

Apolisi agwira mbala zomwe zinaba katundu wa Radio Maria

Apolisi ku Lingadzi mu mzinda wa Lilongwe apeza zipangizo za wailesi ya Radio Maria zimene mbava zinaba masiku apitawa za ndalama yoposa K90 million.

Malinga ndi a Billy Chimbonga amene ndi mkulu wa polisi ya Lingadzi, mbavazo zinathyola kontena yomwe munali zipangizozi, zomwe zinachokera ku Italy, kuti zithandize pokhazikitsa nthambi ina ya Radio Maria ku Area 43 mu mzinda wa Lilongwe.

Pakadali pano, apolisi agwila anthu atatu amene akukhudzidwa ndi nkhaniyi, kuphatikizapo a Chiipira Sato a zaka 50 ochokepa pamudzi wa Kamakoko mdera la Senior Chief Kwataine m’boma la Ntcheu.

Tili pa nkhani ngati yomweyi, apolisi ku Lingadzi komweko akufufuza za mabokosi 450 amatailosi a ndalama zokwana K15 million amene mlonda wina, Richard Patrick Yamu, anaba ku Area 49 kumene abwana ake akumanga nyumba, ndikukagulitsa kwa anthu ena.

Yamu amulamula kuti akakhale kundende kwa zaka zisanu.

Apolisi akwanitsa kupezako mabokosi 164 okha,amene ndi a ndalama zokwana K5 million.

 

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Muslims urged to advocate for peace and stability in Malawi

Sothini Ndazi

Temwa aveka makanda pa chipatala cha Kamuzu Central

Tasungana Kazembe

Apostle Kawinga aids hunger stricken families in CK

Jeffrey Chinawa
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.