A Mapulani Nkosi aku Mzimba akusimba lokoma kaamba kochita ulimi wa mpunga m’bomali, lomwe ambiri amalidziwa ndi ulimi wa fodya komanso mtedza.

A Nkosi, amene ali ndi zaka 34, ati akhala akulima mpunga kwa zaka zitatu tsopano.
“Ine chidwi changa chinabwera pomwe ndinapita ku Karonga kukacheza komwe ndinaona anthu akulima mpunga, ndipo ndinaganiza zophunzirako ziwiri zitatu kuti ndikayesere kwathu,” a Nkosi analongosola.
Nkosi wati atafika kwawo anapeza malo ndikudzala mpunga ndipo pano amakolora ma tini pafupifupi 30.
Pakadali pano, Nkosi wapempha akuluakulu owona za ulimi kumpoto kwa boma la Mzimba kuti ayambe kuthandiza alimi ampunga komanso ena onse omwe aonetsa chidwi ndi ulimiwu ndi upangiri wa momwe angasamalire mbewu zawo komanso kupeza phindu lochuluka.
M’mau ake, mmodzi mwa akuluakulu ku Mzuzu ADD, a Anderson Chikomola, wati ndizopatsa chidwi komanso kulimbikitsa kuona alimi m’bomali akulima mbewu zosiyanasiyana.
Olemba George Mkandawire