Apolisi ku Chiradzulu akufufuza Madalitso Chikondi, wazaka 18, pomuganizira kuti anapha mnzake Innocent Masamba,18 yemwe amamuganizira kuti amazembera chibwenzi chake.
Lovice Mulinde, yemwe ndi wachiwiri kwa ofalitsankhani wa Polisi ya Chiradzulu, wati malemu Masamba anali pasitolo ya Makiliyere komwe amakaonera maimbidwe ena ndipo Chikondi adayamba kumenya ndi kulasa mnzakeyu ndi mpeni ndipo anafera pompo.
Chikondi amachokera m’mudzi wa Mtambo kwa mfumu yayikulu Machinjiri mu mzinda wa Blantyre pomwe Masamba adali ochokera m’mudzi wa Ulaya, kwa mfumu yayikulu Mpama m’boma la Chiradzulu.