Adindo pachipatala cha Nkhotakota apempha anthu akufuna kwabwino kuti athandizepo pamavuto omwe chipatalachi chikukumana nawo monga mwa zina kuchepa kwa zipinda zomwe odwala amagonamo .
Mkulu wa wachipatalachi Dr Jacob Kafulafula anena izi ku Nkhotakota atalandila thandizo la katundu wandalama zoposa K800 miliyoni lomwe bungwe la USAID kudzera muntchito ya Momentum Tikweze Umoyo lapereka m’zipatala zisanu m’dziko muno.
Malinga ndi mkulu wa USAID Momentum, a Marriam Mangochi, ati katunduyu athandizira ana ndi amai omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana .
Polankhulapo Bwanankubwa wa boma la Nkhotakota, a Ben Tohno, ati thandizoli lichepetsa vuto lamayendedwe kaamba koti odwala amayenda mtunda wautali kupita mzipatala zina kaamba kosowa zipangizo zina zogwilira ntchito pachipatalachi.
Ntchito ya USAID Momentum Tikweze Umoyo mothandizana ndi AMREF Health Africa igwiridwa kwazaka zisanu m’maboma asanu m’dziko muno.
Olemba: Aisha Amidu.