Anthu okhala kwa Jumbe ku Machinjiri ati sakumvetsa kuti anamanga malo awo ochitira malonda pamwamba pa paipi yaikulu yamadzi a Blantyre Water Board, katundu ochuluka ataonongeka madzi ataphulika pamalowo.
Pakadali pano, a Blantyre Water Board ali mkati kukonzanso paipiyi, madzi omwe anayenda ngati namondwe atasakaza katundu wandalama zochuluka mu shopuyi.
Mwini malowa, a Guest Tambala, ati nawo mutu waima kamba koti sakumvetsa chomwe chachitikachi.
Olembankhani wathu wati mu shopuyi muli chidzenje chomwe chakumbika ndi madzi ophulikawa, pomwe ogwira ntchito ku BWB akuyesera kukonzanso paipiyi.
Olemba: Mphatso Tebulo