Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Anthu ena akusowabe pokhala – Paramount Chief Kaduya

Mfumu yaikulu ya Alhomwe, Paramount Chief Kaduya, yapempha boma ndi anthu akufuna kwabwino kuti athandizebe pomangira nyumba anthu 1161 amene akusowabe pokhala kutsatira namondwe wa Freddy.

Iwo ayamikira Dr Lazarus Chakwera pokhazikitsa akazembe akufuna kwabwino, omwe ndi Dr Bakili Muluzi ndi Dr Joyce Banda, amene anati awathandiza ndi nyumba zokwana 45.

Iwo athokozanso boma popereka thandizo la chakudya kwa mabanja 38,222 kwa miyezi isanu ndi umodzi 6.

Poyankhulapo, mmodzi mwa anthu omwe anapulumuka pangozi ya madzi pa mudzi wa Ntauchila ku Chiradzulu, mudzi umene onse unapita ndi madzi, a Austin Maloya, anathokoza boma kamba kowamangira nyumba pamudzi watsopano omwe aukhazikitsa ku Mikolongwe m’bomali.

Iwo ati boma lawapatsapo chakudya ndipo chomwe akufuna ndi fetereza komanso mbewu kuti ayambe kulima mwaokha.

 

Blessings Cheleuka

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police nabs ‘King of Street Kids’

Romeo Umali

Komiti yakunyumba yamalamulo yakhutira ndikuthetsedwa kwa mlandu wa a Chilima

Olive Phiri

Malawi media delegation in China for two-week seminar

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.