Nyakwawa yayikulu Gwedeza yaku Ntcheu yati anthu m’bomali ndiwokondwa ndi chitukuko chokulitsa msewu wa M1 pa Kampepuza.
A Gwedeza ati mwachitsanzo, chifukwa cha kuonongeka kwa msewu, pa msika wa Kampepuza pamachitika ngozi zomwe tsopano zikuyembekezeka kuchepa.
Pa Kampepuza ndi amodzi mwa malo odziwika bwino m’boma la Ntcheu kaamba ka msika omwe umachitika lachisanu lililonse.
Ntchito yokonzanso ndikukulitsa msewuwu inayamba mu September chaka chatha ndipo ikuyembekezeka kutha mu November chaka chino.