Ku St Patrick’s Parish, zonse zokonzekera kulandira thupi la Dr Saulos Chilima zatha.
Padakalipano, anthu ochuluka afika kudzakhala nawo pa misa ya maliro a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu.
Malemu Dr Chilima anali mkhristu wa mphamvu wa mpingo wa Katolika wapa Parish ya St Patrick’s ku Area 18.
Ndipo mwa zina, iwo anathandiza nawo pa ntchito yomanga tchalitchi chatsopano cha St Patrick’s.
President wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akuyembekezeka kutsogolera ulendo onyamula thupi ku Goodwill Funeral Services ku Area 4 mu mzinda wa Lilongwe kufika ku St. Patrick’s Parish ku Area 18.
By Isaac Jali