Apolisi ku Lilongwe agwira a Anthony Chimpale a zaka 48 omwe amagwira ntchito kunthambi ya Land Resource and Conservation ku unduna waza malimidwe.
Malinga ndi ofalitsankhani wa apolisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu, zimenezi zachitika mwini ofesi atandaula zakusowa kwa mafoni 75 a mtundu wa Samsung Galaxy tablets, tonner 7, zikwanje zokwana 600; zonse zandalama zokwana K20.9 million pakati pa mwezi wa July 2023 ndi February chaka chino.
Matekitivi apolisi atafufuza zankhaniyi anapeza kuti ena mwa mafoni obedwawa amagwira ntchito mu mzinda wa Lilongwe ndipo anthuwo atawapeza anatchula a Chimpale kuti ndiwo adawagulitsa.
Pamenepa, a Chigalu ati apolisi atawagwira a Chimpale kumathero asabata yathayi, anaulula kuti ndiwo akhala akuba katunduyo ku ofesi pogwilitsa ntchito makiyi omwe adawapeza mwa okha.
Apolisi apezako kale ma foni asanu omwe nthambiyo imasunga podikilira ma polojekiti ake osiyanasiyana mtsogolo ndipo ena 70 akusowabe.
A Chimpale, amene amachokera m’mudzi mwa Nkhwenembera mdera la mfumu Chiwere m’boma la Dowa, akuyembekezeka kukaonekera kubwalo la milandu posachedwapa.