Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Aloleni achinyamata kupereka maganizo ku DPP — Chimwendo Banda

Mtsogoleri wa zokambirana za m’nyumba ya malamulo a Richard Chimwendo Banda ati nthawi yakwana ku chipani cha Democratic Progressive (DPP) kuti apatseko mpata achinyamata popereka maganizo pa zinthu zochitika mchipanichi komanso m’dziko muno.

A Chimwendo Banda ayankhula  izi pamene amadzudzula a Joseph Mwanamvekha omwe ndi m’neneri wa zachuma ku chipani cha DPP kaamba konyazitsa dongosolo la chuma cha boma la chaka cha 2024/25.

A Mwanamvekha ati dongosololi silikupatsa chiyembekezo ati popeza ndalama zakunja zikupitilira kusowa, komanso kuti ngongole za boma zachuluka kwambiri.

Koma a Chimwendo Banda ati n’kosayenera kulankhula monyoza.

 

Olemba Margaret Mapando

Related posts

Mohammad Mokhber ndi mtsogoleri wa dziko la Iran

Romeo Umali

Parliament rise sine die

MBC Online

Form One girl nabbed for stabbing her boyfriend

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.