Banki ya NBS yakhazikitsa mpikisano watsopano wa alimi omwe akuutcha K14 million yonyotsolerana, momwe alimi komanso makasitomala abankiyi adzipata mphotho zosiyanasiyana popikisana kusunga ndalama.
Poyankhula ku Lilongwe pamwambo okhazikitsa mpikisanowu, mkulu owona zamalonda Ku bankiyi, Victoria Chanza, wati mpikisanowu ndimbali imodzi yolimbikitsa mchitidwe osunga ndalama ku banki pakati pa alimi komanso makasitomala ndipo alimi akuyenera kumasunga ndalama kuyambira K500,000 pofuna kulowa nawo.
Mumpikisanowu, omwe ndiwa miyezi itatu, alimi adzipambana mphotho zapamwezi monga mbewu, fertilizer, njinga komanso katundu wina wa bankiyi kupatula ndalama pomwe mmodzi wamphumi adzapate mphotho yaikulu ya K2 million m’mwezi wa September.
Olemba: Foster Maulidi