Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha MCP ku nyumba ya malamulo, a Ulemu Chilapondwa, adzudzula aphungu anyumba ya malamulo kamba ka khalidwe losapereka ulemu kwa Sipikala wa nyumba ya malamulo a Catherine Gotani Hara.
A chilapondwa, omwe ndi phungu wadera la Ntchisi South, anadandaula kuti atatulutsidwa mnyumbayi lachitatu sabata yatha, phungu wadera la Rumphi East, a Kamlepo Kalua, anakalankhula mawu onyoza sipika wanyumbayi pa masamba amchezo.
Poyankhapo pankhaniyi, mtsogoleri wazokambirana mnyumba ya malamulo, a Richard Chimwendo Banda, adandaula komanso kudzudzula khalidwe limene adadonyeza a Kalua, yemwe akuti adanyoza mayi Catherine Gotani Hara polankhula ndi atolankhani sabata yatha.
Wachiwiri kwa sipika wanyumba yamalamulo, a Madalitso Kazombo, anatsindika kufunika kopeleka ulemu kwa mtsogoleri wanyumbayi yemwe ndi sipikala, ponena kuti malamulo a nyumbayi amafotokoza momveka bwino pa nkhani ya ulemu kwa atsogoleri.