Bungwe la Admarc lapatsidwa ndalama zokwana K40 billion kuti liyambenso kugwira ntchito zake modalirika komanso kuyamba kuyendetsa ntchito zake ngati bungwe lochita malonda.
Nduna ya zachuma, a Simplex Chithyola Banda, anena izi pamene akupereka ndondomeko yazachuma ya chaka chaboma cha 2024/2025.
A Banda ati National Food Reserve Agency yapatsidwa K12 billion yogulira chimanga.