Khothi la Magistrate ku Blantyre lalamula apolisi komanso a dipatimenti ya zankhalango kuti apereke galimoto ya mtundu wa Scania yamatani 10 yomwe nambala yake ndi NN 10435 kwa mwini wake patapita nthawi galimotoyi ataigwira pa mulandu wokhudza kuononga zachilengedwe.
Galimotoyi anaigwila apolisi pa 21 December 2023 pa roadblock ya Ngumbe akuyendetsa mwini wake Jonasi Billiat atanyamula matumba a makala.
Malinga ndi zomwe MBC yapeza mkulu wapolisi owona zotengera milandu kubwalo lamilandu omwe ndi wachiwiri kwa komishonala, a Levison Mangani, anapempha bwalo kuti lisapereke galimotoyi kaamba koti mwini wake ndi amenenso anapalamula mlanduwu popezeka akuyendetsa ponena kuti ndiye mbali ina ya umboni waukulu wa boma pa nkhaniyi.
Komabe magistrate amene akuunguza nkhaniyi wapereka galimotoyi kwa a Biliati omwe anakali pa belo yaku khothi pomvela zomwe yemwe amawaimila anafotokozera bwaloli.
Kuyambila chaka chatha apolisi mogwilizana ndi a dipatimenti ya zankhalango komanso bungwe lolimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale akhala akugwira ntchito yothana ndi mchitidwe wosakaza nkhalango pootcha makala.
Bwalo komanso anthu ena omwe akutsatila nkhaniyi anakaona galimotoyo komanso matumba amakalawo kuma ofesi a zankhalango mu mzinda wa Blantyre.
Bwalo la milandu likuyembekezeka kudzamva za nkhaniyi pa 8 February 2024.