Atsogoleri a mipingo ku Likuni ndi kwa Chinsapo ku Lilongwe apereka penti yokwana malita 35 ku Polisi ya Chinsapo Unit kuti akonzere denga limene liri ndi dzimbiri.
Mkulu wa Likuni and Chinsapo Pastors Fraternal, Reverend Daniel Masamba, anati zimakhala zomvetsa chisoni kuona apolisi akupulumutsa katundu wa nkhaninkhani kwambava koma kulephera kupulumutsa denga lawo.
Mkulu wa Polisiyi, a Mavuto Banda, anayamikira chifukwa cha mphatsozi.
M’mbuyomu, atsogoleri a mipingowa anabyzala mitengo pa Polisiyo kaamba kogwira bwino ntchito.
Olemba: Raymond Midaya