Jonathan Phillipo, mneneri wa Polisi ku Chileka
Apolisi ku Chileka amanga bambo McLean Luka a zaka 24 omwe athandiza kuchiritsa okha mkazi wawo yemwe anali oyembekezera, atamukaniza kupita ku chipatala kukalandira chisamaliro choyenera.
Mneneri wa apolisi ku Chileka, Jonathan Phillipo, wati Luka amunjata Senior Chief Kunthembwe ya m’derali itadandaula kuti mwamunayu amaletsa mkaziyu kupita ku chipatala ati polemekeza chipembedzo chake chomwe sichilora kumwa mankhwala mpaka tsiku lobereka mwana, pomwe mkuluyu anamuthandiza yekha.
Mfumuyi inakanena ku polisi omwe anazatengela khandalo ndi mayiyu ku chipatala ku Chileka komwenso anawatumiza awiriwa ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth komwe akulandila thandizo.
Luka amachokera mmudzi mwa Chikoka kwa TA Kunthembwe m’boma la Blantyre.