Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Mwakasungula ati bajeti ili bwino zedi

Mmodzi mwa anthu amene amayankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana, maka zolimbikitsa ulamuliro wabwino, a Undule Mwakasungula, ati dongosolo la zachuma lomwe alipereka mnyumba ya malamulo lachisanu a nduna a zachuma, a Simplex Chithyola Banda, ndi mbambande.

Iwo ati ndondomekoyi ithandiza kutukula miyoyo ya anthu m’dziko muno.

A Mwakasungula anena izi a Banda atapereka ndondomeko yazachuma yachaka chino kufikira chaka chamawa ya ndalama zokwana K5.9 trillion.

A Mwakasungula ati dongosolo latsopanoli laonetseratu kuti boma laika chidwi pantchito yotukula miyoyo ya a Malawi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Athokoza asilamu popemphelera dziko lino mu nyengo ya Ramadhan

Beatrice Mwape

A Mnjale amwalira

Mayeso Chikhadzula

Mukatengera chipani njala ikusautsani, watero Kalitendere

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.