Yemwe anaakhalapo mkulu wa nthambi ya CID, a George Mnjale, amwalira lero ku chipatala cha Kamuzu Central mumzinda wa Lilongwe kumene amalandira thandizo.
A Mnjale amwalira ali pa udindo wa wachiwiri kwa komishonala wa apolisi (Deputy Commissioner of Police).
Iwo anabadwa pa 24 October, 1970 ndipo amachokera m’boma la Dowa.
#MBCDigital
#Manthu