A Jacob Hara, omwe ndi nduna ya za mtengamtenga, apempha anthu m’dziko muno kuti akhale odekha pamene boma likuyesetsa kukonzanso misewu.
Ndunayi yayakhula izi pomwe imayendera ntchito yomanga komaso kukonza msewu wa M1, kuchoka pa mphambano yopita ku Kamuzu International Airport ku Lilongwe kufika ku Kasungu mpaka kwa Jenda.
A Hara ati ndiokhutira ndi momwe ntchito yomanga msewuyi ikuyendera.
Mmodzi mwa akuluakulu ku Roads Authority, Engineer Joe Longwe, ati akulondoloza bwino lomwe nthawi yomwe anapatsana ndi ma kontrakitala omanga misewu ndi cholinga choti misewu ikhale yapamwamba.