Phungu wa nyumba yamalamulo wadera la kuzambwe kwa boma la Mulanje, a George Chaponda, amene awathamangitsa ku msonkhano wa akuluakulu a ku nyumba ya Malamulo komwe amafuna kukaimira ngati mtsogoleri wa aphungu otsutsa pa zokambiranazo, tsopano ali ku msonkhano wa bungwe la Democracy Works Foundation komwe akuimiranso chipani cha DPP.
Bungwe la Democracy Foundation lakonza maphunzirowa pofuna kupereka upangiri kwa akuluakulu a zipani zisanu ndi chimodzi zimene zili ndi aphungu mu nyumba ya malamulo pa zomwe akuyenera kuchita ndi kutsata pa ndondomeko yaza chuma yomwe aikambirane ku nyumba ya malamulo.
Poyankhula pozizindikiritsa, a Chaponda auza msonkhanowu kuti iwo ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo chakummwera.
Iwo awathamangitsa ku msonkhano oyambawo kumene akuluakulu a ku nyumba ya malamulo akukambirana mmene mkumano wa nyumba ya Malamulo, umene uyambe lachisanu, uyendere.
Wolemba: Beatrice Mwape