Phungu wadera la kumpoto m’boma la Karonga, a Mungasulwa Mwambande, wati chimene chachititsa kuti alowe chipani cha Malawi Congress (MCP) ndi zitukuko zimene President Dr Lazarus Chakwera akumwaza m’dziko muno mosayang’ana dera kapena zigawo.
A Mwambande, amene amayankhula ku Iponga pa msonkhano wandale powalandira m’chipanichi, ati anthu ochuluka mdera lawo ndi okondwa ndi utsogoleri umene ulipo pano, moti akufuna upitilire mpakana 2030 kuti dziko lino likhale losinthika.
Iwo anali a chipani cha Democratic Progressive ndipo anakhalapo wachiwiri kwa nduna yoona za migodi.
Mlembi wa chipani cha MCP, a Richard Chimwendo Banda, yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowu, anamema anthu kuti akhale pambuyo pa Dr Chakwera, omwe cholinga chawo ndi kusintha miyoyo ya anthu onse m’dziko muno.
Olemba: Musase Cheyo
Ojambula: Boston Tembo