Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

A Chakwera alibe tsankho — Chimwendo Banda

Nduna ya maboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe, yomwenso mkulu woona za achinyamata mchipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, yati boma la Dr Lazarus Chakwera likulimbikitsa umodzi m’dziko muno.

Poyankhula pa msika wa Zigwagwa pomwe Prezidenti Chakwera anayankhula ndi khwimbi lomwe linasonkha atamaliza kuyendera msika wa Mzuzu Flea market komanso wa Zigwagwa, a Chimwendo Banda anati Dr Chakwera alibe tsankho pochita zitukuko mdziko muno.

Iwo anati mwa zina, nduna za boma komanso akuluakulu ena aboma ndi wochokera m’chigawo chakumpoto, zomwe zikuonetsa poyera kuti ali ndi mtima wolorena.

Iwo anatchulapo zakudzipereka kwa boma pokhazikitsa zitukuko zosiyanasiyana m’dziko monse muno.

Pa nkhani ya ndale, a Chimwendo Banda anati khomo la chipani cha MCP ndi lotsekula ndipo mchifukwa chake anthu ambiri akulowa mchipanichi.

Iwo anatchulapo za a Joe Nyirongo, a Ken Msonda, a Werani Chilenga onse omwe achoka ku chipani chotsutsa cha DPP.

A Chimwendo Banda anayamikanso Dr Chakwera chifukwa chothetsa mchitidwe wokondera pa maphunziro wa quota system.

Dr Chakwera ali mchigawo chakumpoto komwe akuyendera ntchito zosiyanasiyana zachitukuko.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

GOVERNMENT REDUCES THE PRICE OF PETROL

McDonald Chiwayula

Tripartite nations gather to boost trade relations

Alinafe Mlamba

Donors pledge $50 million towards Malawi’s agriculture sector

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.