Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati ndi kofunika kuti chitetezo chikhale chokhwima pofuna kuthana ndi atambwali amene amazembetsa fodya kupita naye ku maiko akunja posafuna kulipira msonkho.
Dr Chakwera amayankhula izi m’boma la Kasungu potsegulira msika wa malonda a fodya ndipo anati lamulo ligwire ntchito pa mchitidwewu
“Tikupempha inu a Inspector General kuti gwirani tchito yothana ndi anthu amenewa,” anatero Dr Chakwera.
Mtsogoleriyu anayamikiranso ntchito yotamandika yomwe alimi a fodya akugwira pothandizira kuti dziko lino lidzipeza ndalama zakunja (forex).
Dr Chakwera alangiza anthu onse kuti azidzipereka pa ntchito zosiyanasiyana zothandiza kuti dziko lino lidzipeza ndalama zakunja ngati momwe akuchitira alimi a fodya.