Zadziwika kuti amayi ambiri sakonda kugwiritsa ntchito makondomu achizimayi zomwe zikupangitsa kuti makondomu-wa adziwonongeka asanagwiritsidwe ntchito.
Wanena izi ndi mkulu owona zopewa kufala kwa kachirombo ka HIV wa bungwe la Aids Healthcare Foundation (AHF) kuchigawo chakum’mwera, a Jacob Pidini.
Iwo amafotokoza izi pamwambo wa tsiku lokumbukira kufunika kwa kondomu popewa kutenga mimba zosayembekezera, kutenga matenda opatsirana pogonana kuphatikizapo HIV.